Panopa ndimagwira ntchito ya ulonda koma ndalama yomwe ndimalandira sikwanila kugura njinga yamoto ya brand new,koma nditawina ndalama imenei nditha kuyamba business ya kabaza imenei ,panopa kunoko anthu amakwera njinga zamoto kwambiri ndikhumbo langa kukhala ndinjinga yamoto yanga yanga ndithu, ndimaona nthawi zambiri ndikabwereka njinga ya zanga pa Sunday ndimapanga ndalama ndithu kukwanisa kugura chakudya pakomo...