Bizinesi yanga ndi yogulitsa zovala za bale za abambo, amayi ndi ana. Timasankha zovala zabwino, zoyera komanso zamafashoni amasiku ano kuchokera ku mabello osiyanasiyana. Timagulitsa pa sitolo yaying'ono komanso kudzera pa Facebook, WhatsApp ndi TikTok. Makasitomala amatha kubwera kusitolo kapena timawatumizira kunyumba. Cholinga chathu ndikupatsa anthu zovala zabwino zamtengo wotsika kuti aliyense azivala bwino...