Ndili ndi lingaliro loyambitsa business yotchedwa Mlimi Fresh Market, yomwe ndidzakhala ndikugulitsa zipatso ndi ndiwo zamasamba zatsopano. Cholinga changa ndi kupanga malo kapena njira yosavuta yomwe anthu angapezere zipatso ndi ndiwo zamasamba zathanzi komanso zatsopano pamtengo wokwanira. Ndikukonzekera kuti mtsogolomu ndizipeza zipatso ndi ndiwo zamasamba kuchokera kwa alimi osiyanasiyana, komanso kulima zina...