Ndili ndi malo omwe ndinagalauzapo cholinga nthawi yamvura ikamakwana ndidzalepo mpendadzuwa kuti ndizitha kudzithqndiza ine mwini komanso abale ndi anthu ena mudzi mwathu. Mpendadzuwa amathandiza munjira zosiyanasiyana monga kugwiritsa ntchito ngati mafuta ophikira tikasikinya kapena kuti kumunyenya pa chipangizo chonyenyera mpendadzuwa pamene takolola