Rabbits Farm ndi business yomwe ndikufuna kuyambitsa yoweta akalulu, makamaka kubereketsa ndi kuweta akalulu athanzi kuti ndizigulitsa ngati nyama komanso akalulu obereketsa. Ndiyamba ndi akalulu abwino obereketsa ndipo ndidzawapatsa malo abwino, chakudya chokwanira, madzi oyera, ukhondo komanso chisamaliro cha thanzi. Akalulu amakula mwachangu ndipo amatha kufika pa msinkhu wogulitsidwa pafupifupi miyezi 2–3...