Business yanga ikayambika, cholinga chake chachikulu ndi kupanga ntchito yojambula zithunzi ndi mavidiyo kwa anthu, mabizinesi, masukulu, mabungwe komanso pa zochitika zosiyanasiyana. Ntchitoyi ithandiza anthu kuti azitha kusunga ndi kufalitsa zochitika zawo pogwiritsa ntchito zithunzi ndi mavidiyo abwino komanso amakono. Businessyi iperekanso mwayi kwa achinyamata kuti aphunzire luso la photography, videography...